Awa ndi mayeso oyesedwa. Apambaneni kuti mupeze mfundo zopita ku Satifiketi ya Chivomerezo cha Utumiki yanu.
AHEBRI 5:14 — Koma chakudya cholimba ndi cha anthu okhwima msinkhu, amene pogwiritsa ntchito nzeru zawo, aphunzira ________ chabwino ndi choyipa.
kusiyanitsa
kupitiriza
utumiki
2 AKORINTO 11:3 — Koma ndikuopa kuti monga Hava ananyengedwa ndi ________ kwa njoka, mitima yanunso ingasocheretsedwe kuleka nʼkudzipereka moona mtima ndi modzipereka kwenikweni kwa Khristu.
mayesero
kuchenjera
cholemetsa
AROMA 6:23 — Pakuti ________ a tchimo ndi imfa, koma mphatso yaulere imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha mwa Khristu Yesu Ambuye athu.
malipiro
mdani
Atate
1 YOHANE 2:16 — Pakuti zonse za mʼdziko lapansi, ________ za thupi, zinthu zimene maso amakhumbira ndiponso kuyandikira zinthu za moyo uno, zonsezi sizichokera kwa Atate, koma ku dziko lapansi.
ochimwa
kubweretsa
zilakolako
GENESIS 3:22 — Ndipo Yehova Mulungu anati, “Tsopano munthu uyu wasanduka mmodzi wa ife, wodziwa zabwino ndi zoyipa. Iyeyu asaloledwe kutambasula dzanja ndi kutengako ________ za mu mtengo wopatsa moyo uja kuti angakhale ndi moyo mpaka muyaya.”
woyamba
zipatso
mlendo
MARKO 7:21 — Pakuti kuchokera mʼkati mwa mitima ya anthu, mumatuluka maganizo oyipa, chiwerewere, kuba, kupha, ________
chigololo
mtsikana
dera
YEREMIYA 4:22 — Yehova akuti, “Anthu anga ndi ________; iwo sandidziwa. Iwo ndi ana opanda nzeru; samvetsa chilichonse. Ali ndi luso lochita zoyipa, koma sadziwa kuchita zabwino.”
zitsiru
njoka
mikango
MALAKI 2:17 — Mwamutopetsa Yehova ndi zoyankhula zanu. Inu mukufunsa kuti, “Kodi tamutopetsa bwanji?” Mwamutopetsa ponena kuti, “Aliyense amene amachita zoyipa ndi wabwino pamaso pa Yehova ndipo iye ________ naye” kapena pofunsa kuti, “Ali kuti Mulungu woweruza mwachilungamo?”
amadalira
chigololo
amakondwera
YESAYA 7:15 — Azidzadya ________ ndi uchi, mpaka atadziwa kukana choyipa ndi kusankha chabwino.
chikhomo
chambiko
matope
MASALIMO 97:10 — Iwo amene amakonda Yehova adane ndi zoyipa pakuti Iye amayangʼanira ________ ya amene amamukhulupirira ndipo amawapulumutsa mʼdzanja la anthu oyipa
mʼmabwalo
mabala
miyoyo
1 MAFUMU 3:9 — Choncho mupatseni mtumiki wanu nzeru zolamulira anthu anu ndi kuti azitha ________ pakati pa chabwino ndi choyipa. Pakuti ndani amene angathe kulamulira anthu anu ochulukawa?”
1 ATESALONIKA 5:22 — ________ choyipa cha mtundu wina uliwonse.
pachiswe
Mupewe
cholemetsa
AROMA 16:19 — Aliyense anamva za ________ kwanu, choncho ndine odzaza ndi chimwemwe chifukwa cha inu. Koma ine ndikufuna kuti inu mukhale anzeru pa zabwino, ndi wopanda cholakwa pa zimene zili zoyipa.
chilango
chikondi
kumvera
MACHITIDWE A ATUMWI 10:38 — kuti Mulungu, anamudzoza Yesu, wa ku ________ ndi Mzimu Woyera ndi mphamvu ndiponso mmene Iye anapita nachita zabwino ndi kuchiritsa onse amene anali pansi pa mphamvu ya mdierekezi, popeza kuti Mulungu anali naye.
Nazareti
Tarisisi
Damasiko
1 PETRO 3:11 — Apewe zoyipa, ndipo azichita zabwino. Afunefune ________ ndi kuyesetsa kuwupeza.
chikondi
mtendere
Mzimu
AROMA 12:21 — Musagonjetsedwe ndi choyipa, koma gonjetsani choyipa ________ chabwino.
kumvera
chilango
pochita
MASALIMO 34:14 — Tembenuka kuchoka ku zoyipa ndipo chita zabwino; funafuna ________ ndi kuwulondola.
AROMA 5:19 — Pakuti kusamvera kwa munthu mmodzi kunasandutsa anthu ambiri kukhala ________, chimodzimodzinso anthu ambiri adzasanduka olungama kudzera mwa munthu mmodzinso.
zilakolako
ochimwa
ziwanda
1 PETRO 2:24 — Iye mwini anasenza machimo athu mʼthupi lake pa mtanda, kuti ife tife kutchimo ndi kukhala ndi moyo potsata chilungamo, ndipo ndi ________ ake munachiritsidwa.
miliri
mabala
mapemphero
CHIVUMBULUTSO 2:7 — Amene ali ndi makutu, amve zimene Mzimu akuwuza mipingo. Amene adzapambana, ndidzamupatsa ufulu wakudya ________ za mtengo wopatsa moyo umene uli ku paradizo wa Mulungu.
chikondi
yekha
zipatso
CHIVUMBULUTSO 22:2 — Ukuyenda pakati pa msewu waukulu wa mu mzindawo. Mbali iliyonse ya mtsinjewo kunali mtengo wamoyo, utabala zipatso khumi ndi ziwiri. Kubereka zipatso mwezi uliwonse. Ndipo masamba a mtengowo ndi ________ wochiritsa anthu a mitundu ina.