YAKOBO 5:7 — Tsono abale, pirirani mpaka kubwera kwa Ambuye. Onani mmene amachitira mlimi. Amadikirira kuti ________ zabwino zioneke mʼmunda mwake. Amayembekezera mokhazikika mtima kuyambira nthawi ya mvula yoyamba mpaka yotsiriza.
chisomo
chuma
zipatso
YAKOBO 5:11 — Monga mukudziwa, tinawatenga ngati odalitsika anthu amene anapirira. Munamva za kupirira kwa ________ ndipo mwaona zimene Ambuye anamuchitira potsiriza pake. Ambuye ndi wodzaza ndi chisoni ndi chifundo.
Aramu
Yese
Yobu
AROMA 15:4 — Pakuti zilizonse zimene zinalembedwa kale zinalembedwa kuti zitiphunzitse ife. Malembawo amatilimbikitsa kupirira kuti tikhale ndi ________.
thupi
chiyembekezo
wolungama
AROMA 15:5 — Mulungu amene amapereka kupirira ndi chilimbikitso akupatseni ________ amodzi pakati panu monga inu mukutsatira Khristu Yesu
maganizo
magulu
mizinda
AKOLOSE 1:11 — Timapempheranso kuti Mulungu akulimbikitseni ndi mphamvu yake yonse ya ulemerero wake, kuti muzipirira zonse ndi mitima yofatsa ndi ya ________