MASALIMO 94:10 — Kodi Iye amene amalangiza ________ ya anthu sangathenso kulanga? Kodi Iye amene amaphunzitsa munthu angasowe nzeru?
nsembe
mitundu
phiri
HOSEYA 6:3 — Tiyeni timudziwe Yehova, tiyeni tilimbike kumudziwa Iye. Adzabwera kwa ife mosakayikira konse ngati kutuluka kwa ________; adzabwera kwa ife ngati mvula ya mʼchilimwe, ngati mvula ya nthawi yamphukira imene imakhathamiritsa nthaka.”
phiri
khomo
dzuwa
YOHANE 7:17 — Ngati munthu asankha kuchita chifuniro cha Mulungu, adzazindikira ngati ________ changa nʼchochokera kwa Mulungu kapena ngati ndi mwa Ine ndekha.
mlongo
bwenzi
chiphunzitso
MATEYU 11:29 — Senzani ________ langa ndipo phunzirani kwa Ine, pakuti ndine wofatsa ndi wodzichepetsa. Ndipo inu mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu.
pemphero
goli
mlongo
2 PETRO 3:18 — Koma kulani mu ________ ndi mʼchidziwitso cha Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu. Kwa Iye kukhale ulemerero tsopano mpaka muyaya. Ameni.
chisomo
thupi
chiyembekezo
2 PETRO 1:5 — Choncho, chitani khama kuwonjezera moyo wabwino pa ________ chanu, ndipo pa moyo wabwino muwonjezerepo nzeru.
chikhulupiriro
chisomo
chiyembekezo
MIYAMBO 10:14 — Anzeru amasunga ________ koma pakamwa pa chitsiru pamatulutsa zowononga.
chiyembekezo
mphotho
chidziwitso
MIYAMBO 15:14 — Mtima wa munthu wozindikira zinthu umafunafuna ________, koma pakamwa pa zitsiru pamadya uchitsiru wawo.
nzeru
chuma
chakudya
AKOLOSE 1:9 — Chifukwa cha ichi, kuyambira tsiku limene tinamva za inu, sitinasiye kukupemphererani ndi kumupempha Mulungu kuti akudzazeni ndi ________ cha chifuniro chake kudzera mu nzeru yonse yauzimu ndi kumvetsetsa.
chiyembekezo
chisomo
chidziwitso
AKOLOSE 1:10 — Ndipo tikupempherera zimenezi ndi cholinga chakuti inu mukhale moyo oyenera Ambuye ndi kumukondweretsa mʼnjira zonse. Kubereka chipatso pa ntchito iliyonse ________, ndi kukula mʼchidziwitso cha Mulungu.
yabwino
okondedwa
mwamphamvu
AFILIPI 1:9 — Ndipo pemphero langa ndi lakuti chikondi chanu chipitirire kukulirakulira pa ________ ndi kuzama mʼmaganizo
chidziwitso
chiyembekezo
kuyambira
1 AKORINTO 8:1 — Tsopano za chakudya choperekedwa nsembe kwa ________: Ife tidziwa kuti tonse tili ndi chidziwitso. Komatu chidziwitso chokha chimadzitukumula, koma chikondi ndicho chimapindulitsa.
malamulo
malangizo
mafano
MIYAMBO 3:6 — Pa zochita zako zonse uvomereze kuti Mulungu alipo, ndipo Iye adzawongola ________ zako.
malangizo
nkhosa
njira
MASALIMO 119:66 — Phunzitseni nzeru ndi chiweruzo chabwino, pakuti ndimakhulupirira ________ anu.
2 AKORINTO 4:6 — Pakuti Mulungu amene anati, “Kuwala kuwunike kuchokera mu ________,” Iyeyo ndiye anawunikira mʼmitima mwathu kutipatsa kuwala kuti tidziwe ulemerero wa Mulungu umene ukuoneka pa nkhope ya Yesu Khristu.
malangizo
mdima
chilungamo
AEFESO 6:17 — Valani ________ cha chipulumutso ndi kutenga lupanga la mzimu, limene ndi Mawu a Mulungu.
chipewa
ubatizo
zauzimu
MALAKI 2:7 — “Pakuti wansembe ayenera kukhala ndi chidziwitso, ndipo anthu ayenera kufunafuna malangizo kuchokera kwa iye, popeza iye ndi mthenga wa Yehova ________.
Wamphamvuzonse
nsembe
mitundu
MIYAMBO 15:2 — Munthu wanzeru amayankhula zinthu za nzeru, koma pakamwa pa ________ pamatulutsa za uchitsiru.
malamulo
ochimwa
zitsiru
1 PETRO 3:15 — Koma lemekezani Khristu mʼmitima mwanu ngati Ambuye wanu. Khalani okonzeka nthawi zonse kuyankha aliyense amene akufunsani za ________ chimene muli nacho.