MATEYU 10:28 — Musamaope amene amapha thupi koma sangathe kuchotsa moyo. Koma muziopa Iye amene akhoza kupha mzimu ndi kuwononga thupi mu ________.
gehena
mphatso
mʼbusa
MACHITIDWE A ATUMWI 9:31 — Pamenepo mpingo wa ku ________ konse, ku Galileya ndi ku Samariya unakhala pamtendere, unalimbikitsidwa; ndi kupatsidwa mphamvu ndi Mzimu Woyera, unakula mʼchiwerengero, ndi kukhala moopa Ambuye.
Yudeya
Asiya
Damasiko
2 AKORINTO 7:1 — Abwenzi okondedwa, popeza tili ndi ________ amenewa, tiyeni tidziyeretse, kusiyana nazo zilizonse zimene zikhoza kudetsa thupi ndi mzimu, ndipo tiyesetse kukhala oyera mtima poopa Mulungu.
zilakolako
mayesero
malonjezo
AFILIPI 2:12 — Tsono, ________ anga okondedwa, monga mwakhala omvera nthawi zonse, osati pamene ndinali nanu pokha, koma tsopano koposa pamene ndili kutali. Pitirizani kugwira ntchito ya chipulumutso chanu mwa mantha ndi kunjenjemera